
‘Isa bin ‘Umailah (Rahimahullah) akufotokoza za munthu wina amene adawona khalidwe la Abu Zar (Radhwiyallahu ‘anhu) kwa anansi ake ndi alendo. Akunena kuti:
“Nthawi iliyonse Abu Zar radhwiyallahu anhu akamakama mkaka wa mbuzi zake, poyamba ankagaira mkakawu anthu oyandikana nawo nyunba ndi alendo ake kuti ayambe amwa iwowo kenako ankamwa iyeyo.”
Usiku wina, ndinamuona Abu Zar akukama mbuzi zake mkaka mpaka kufika poti udasiya kutuluka m’mabere. Kenako anapereka mkakawo kwa alendo ake ndipo anawaikiranso tende ochepa ndikuwapatsa.
Pambuyo pake anawapepesa chifukwa chosawapatsa china chilichonse choti adye chifukwa analibe china chilichonse panthawiyo, anawalankhula nati, “Tikanakhala ndi china chabwino kuposa ichi, tikadakupatsani.”
Ndinamuona Abu Zar usiku umenewo kuti anagona ndi njala sanadye ngakhale chidutswa chimodzi koma anapereka chilichonse chomwe anali nacho kwa alendo ake. (Siyar A’laam min Nubalaa’ 3/399)
Alislaam Juhudi za Kuleta uislam ndani ya maisha yetu